KUKHAZIKITSIDWA KWA MA GALIMOTO ZIKULUZIKULU (MA THILAKI) ZA A IVECO

Anthu ambiri maka ku Middle East akhala akugwiritsa ntchito galimoto zikuluzikulu za manual pochitira malonda ndikunyamulira katundu wosiyanasiyana. Pakupita kwa nthawi, ma kampani opanga galimoto anayamba kukonza galimoto zikulu zikulu za engine ya automatic ndipo pano anthu ayamba kuwona ubwino wa galimotozi

Kamba ka ichi, kampani yopanga galimoto ya Iveco posachedwapa inakhazikitsa mtundu wagalimoto yayikulu yotchedwa Trakker Eurotronic pamwambo womwe kampaniyi idaakonza limodzi ndi a Saeed Mohammed al Ghandi & Sons (SMAG) aku United Arab Emirates(UAE) ku Motor city ku Dubai. Pamwambopo panafika anthu oposa 150 kuyimilira mizinda, ma kampani a zomangamanga, za maulendo ndi ena.

Pa mwambopo padaonetsedwa galimoto zikuluzikulu zosiyanasiyana kuphatikizapo Trakker Eurotronic. Anthu omwe adabwera kumwambowo anapatsidwa mpata woyeza galimotozo kuti adziwonere wokha ubwino wake.

Kupatula Trakker Eurotronic , galimoto zina za kampani ya Iveco monga Eurocargo ndi Newdaily zinawonetsedwanso pamwambowo.

Kubwera kwa ma gearbox a automatic a galimoto zazikulu kukudza pomwe anthu ambiri pa dziko lonse akufunitsitsa kumagwiritsa ntchito galimoto zotetezeka komanso zosavuta kugwiritsa ntchito.

“tsopano tizigwiritsa ntchito galimoto zosaboola mthumba zikaonongeka komanso zosavuta kugwiritsa ntchito. Izi zitithandiza kuchepetsa ndalama zomwe timaononga kukonzetsera galimoto zazikulu zikaonongeka”-anafotokoza motero a Graham Turner, mkulu wa kampani ya Al Ghandi Auto.

Turner anati dziko lonse la United Arab Emirates likufunitsitsa kuti chitetezo cha pansewu chichuluke pa galimoto zikuluzikulu.

“Tawonapo boma likulimbikitsa ma kampeni osiyanasitana kuti ntchito za chitetezo cha pansewu zipite patsogolo ndiye kubwera kwa galimotoza za makonozi kuthandiza kuti zinthu zambiri zipite patsogolo.”- Anatero a Turner

Malinga ndi mkulu owona za malonda ku kampani ya Iveco ku dera la Africa komanso ku Middle East a Luca Sra, ntchito yokonza galimoto za engine za utomatic inayamba pakati pa zaka 10 ndi 15 zapitazo.

“Anzathu amayiko aku ulaya monga uk,Germany ndi France anayamba kalekale kugwiritsa ntchito engine za mtunduwu ndipo zinafalikira mmayiko ena aku Ulaya ndipo pano zabwera kudzakhazikika kuno.” Anafotokoza motero a Sra.

Sra anati “galimoto zatsopanozi zithandiza ma kasitomala a Iveco kamba koti galimotozi ndizodalilika ndipo zimamwa bwino mafuta”

Ma engine atsopanowa akhoza kugwiritsidwa ntchito mpaka pamapeto kapena pang`onopang`ono. Ma Gear box ake amayesedwa mmalinga ndi kulemera kwa katundu,mmene nsewu uliri komanso mmene galimoto ikuyendetsedwera kuti munthu adziwe mmene galimotoyo ikugwirira ntchito komanso mmene ikumwera mafuta

Malinga ndi a Sra, ma gearbox a Eurotronic anapangidwa mothandizana ndi kampani ya ZF omwe anasankhidwa kuti athandize kampani ya Iveco pogwira ntchito yokonza ma Gearbox amakonowa

TRAKKER

Galimoto yatsopanoyi imatha kunyamula katundu wa ma tani 18 kulekeza 41 komanso nthawi zina imafika mpaka ma tani 70. Ma dalaivala oyendetsa galimoto yatsopanoyi azitha kuyendetsa galimotoyi mosangalala ndi momasuka kamba koti ili ndi mpando wabwino wokhalira womwe ukhozanso kuthyoledwa kuti munthu atha kugona nthawi yomwe akupumulagalimoto litayima.

A Sra anatinso dera la Africa ndi Middle East lakula kwambiri pankhani za malonda ndipo ndi limodzi mwa madera omwe akugula kwambiri ma Trak a kampani ya Iveco. Iwo anati ma ma thilaki-wa amagwiritsidwa ntchito mmisika ya mayiko a pakati mu Africa monga Djibout,Ethiopia,Nigeria ndi Angola.

Ku United Arab Emirates komanso ku Qutar, galimotozi zikugulidwa kwambiri maka kwambiri kamba ka ntchito za zomangamanga zomwe zikuchitika mmayikowa.

A Graham Turner anati ntchito zomwe zikuchitika komanso zina zomwe zikudza kutsogoloku monga ya Expo 2020 ku Dubai, ichititsa kuti dziko la United Arab Emirates likhale kasitomala wamkulu wa kampani ya Iveco.

“Mzodziwikiratu kuti padakali pano nsika wathu siwuli bwino kwenikweni koma tiri ndi chiyembekezo kuti pomafika chaka cha 2020 zinthu ziyamba kutiyendera bwino pa nsika. Pachifukwachi, tikuyesetsa kuwonetsetsa kuti tiri ndi chirichonse kuyambira ma Van mpakana ma Truck komanso kuwonetsetsa kuti takhazikitsa misika yathu mmalo ambiri

Ngakhale galimoto za Euro 3 zikupezeka zambiri pansika, mkulu wa kampani ya Iveco kudera la Gulf, Marco Torta wati anthu ambiri akhala akuvutitsa kupempha kuti ma Thilaki a Euro 5 apezekenso pansika.

“Nkhawa yokhayo yomwe tiri nayo ndiyakuti mafuta agalimotozi ndiwosowa kuno ku United Arab Emirates. Komabe, tikuyesetsa kuti mafutawa adzipezeka ndipo mtsogolomu tidzakhala ndi galimoto zambiri za Euro 5.

Kampani ya Iveco yatinso ikuyesetsa kupeza njira zina zothandizira kuti mafuta a galimotozi apezeke mosavuta kuti ma Euro 5 ayambe kupezeka paliponse mosavuta.

MAPHNZIRO A MAKASITOMALA

Ndikovuta kuti kampani yopanga galimoto ikulitse msikawake ngati ilibe ndondomeko zabwino zochititsa kuti makasitomala azisangalala ndi zintchito zake. Kwa kampani ya Iveco komanso SMAG, ndondomeko yayikulu yofunikira ndiyo kuchititsa maphunziro kwa anthu ogula komanso ogulitsa ga;imoto.

Kampani ya SMAG inakhzikitsa malo ake ndicholinga chophunzitsa anthu mmene angakonzere komanso kusamala galimoto zawo. Kampani ya Iveco imagwiritsa ntchito malo omwewa kuchititsa maphunziro a makasitomala, anthu okonza galimoto ndi ene otero. Kampaniyi imachititsanso ma phunziro kwa anthu osiyanasiyana kuti athe kuzindikira bwino zambiri zokhudza zinthu zomwe kampaniyi imapanga.

“Anthu amachoka mmayiko monga Saudi Arabia ndi Kuwait kuti adzalandire maphunziro osiyanasiyana okhudza zinthu zomwe timapanga. Timachita izi kamba koti timadziwa kuti ngati kasitomala aphunzitsidwa momwe angasamalilire katundu wathu, nde kuti tsiku lina adzabweranso kudzagula katundu wathu. Chiyambireni kuphunzitsa ma kasitomala komanso ma driver, zathandizia kwambiri kukhala ndi ubale wabwino ndi makasitomala athu,” anayankhula motero a Sra.

"Titangoyamba kuphunzitsa madarayiva madarayivawo a ayamba kuona ubwino wamaphunzirowo chifukwa anaona kutsintha, mafuta a ayamba kutupa, Madura ananda kutupa ndi 5 mpaka 15%." Eni ake amagalimoto sadathe kumvesa izi.

Source : Me Construction News